11. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
12. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mkazi wa mwini akapatukira mwamuna wace, nakamcitira mosakhulupirika,
13. ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wace, ndikumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwira alimkucita;
14. ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti acitire nsanje mkazi wace, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amcitire mkazi wace nsanje angakhale sanadetsedwa;
15. pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wace kwa wansembe, nadze naco copereka cace, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo libano; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yacikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.
16. Ndipo wansembe abwere naye, namuike pamaso pa Yehova;
17. natenge madzi opatulika m'mbale yadothi wansembeyo, natengeko pfumbi liri pansi m'kacisi, wansembeyo nalithire m'madzimo.