14. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'cipululu ca Sinai, nati,
15. Werenga ana a Levi monga mwa nyumba ya makolo ao, monga mwa mabanja ao; uwawerenge mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu.
16. Ndipo Mose anawawerenga monga mwa mau a Yehova, monga adamuuza.
17. Ndipo ana a Levi maina ao ndi awa: Gerisoni, ndi Kohati ndi Merari.
18. Ndi ana a Gerisoni maina ao ndi awa, monga mwa mabanja ao: Libini, ndi Simei.
19. Ndi ana a Kohati monga mwa mabanja ao: Amiramu ndi lzara, Hebroni ndi Uziyeli.
20. Ndi ana a Merari monga mwa mabanja ao: Mali ndi Musi. Awa ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.