Ndipo Moabu anati kwa akuru a Midyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse ziri pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Moabu masiku amenewo.