Ndipo buruyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m'njira, ndi lupanga lace ku dzanja lace; ndi buru anapatuka m'njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda buru kumbwezera kunjira.