Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwace mwazi wace pa guwa la nserobe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya pfungo lokoma kwa Yehova.