1. Koma Kora, mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;
2. ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna: mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israyeli, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka.
3. Ndipo anasonkhana motsutsana pa Mose ndi Aroni, nanena nao, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pao; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?
4. Pamene Mose anamva ici anagwa nkhope yace pansi;
5. nanena ndi Kora ndi khamu lace lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ace ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa iye.