1. Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi mota wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku cilekezero ca cigono.
2. Pamenepo anthu anapfuulira kwa Mose; ndi Mose anapemphera kwa Yehova, ndi motowo unazimika.
3. Ndipo anacha malowo dzina lace Tabera; popeza moto wa Yehova udayaka pakati pao.
4. Ndipo anthu osokonezeka ali pakati pao anagwidwa naco cilakolako; ndi ana a Israyeli omwe analiranso, nati, Adzatipatsa nyama ndani?
5. Tikumbukira nsomba tinazidya m'Aigupto cabe, mankaka, ndi mavwendi, ndi anyesi a mitundu itatu;
6. koma tsopano moyo wathu waphwa; tiribe kanthu pamaso pathu koma mana awa.
7. Ndipo mana ananga zipatso zampasa, ndi maonekedwe ace ngati maonekedwe a bedola.
8. Anthu amamka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.
9. Ndipo pakugwa mame pacigono usiku, mana anagwapo.
10. Ndipo Mose anamva anthu alikulira m'mabanja ao, yense pakhomo pa hema wace; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose.