Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkuru. Nabvomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi.