Pamenepo anati, Tidzawabwezera osawalipitsa kanthu, tidzacita monga momwe mwanena. Pamenepo ndinaitana ansembe, ndi kuwalumbiritsa, kuti adzacita monga mwa mau awa.