Koma kunacitika mwezi wa Nisana, caka ca makumi awiri ca Aritasasta mfumu pokhala vinyo pamaso pace, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wacisoni pamaso pace ndi kale lonse.