Ndipo iwo anasunga udikiro wa Mulungu wao, ndi udikiro wa mayeretsedwe; momwemonso oyimbira ndi odikira, monga mwa lamulo la Davide ndi la Solomo mwana wace.