1. Wophwanyayo wakwera pamaso pako; sunga linga, yang'anira panjira, limbitsa m'cuuno mwako, limbikitsatu mphamvu yako.
2. Pakuti Yehova abwezeranso ukulu wace wa Yakobo ngati ukulu wace wa Israyeli; pakuti okhuthula anawakhuthula, naipsa nthambi zace za mpesa.
3. Zikopa za amphamvu ace zasanduka zofiira, ngwazi zibvala mlangali; magareta anyezimira ndi citsulo tsiku la kukonzera kwace, ndi mikondo itinthidwa.
4. Magareta acita mkokomo m'miseu, akankhana m'makwalala; maonekedwe ao akunga miuni, athamanga ngati mphezi.
5. Akumbukila omveka ace; akhumudwa m'kupita kwao, afulumira ku linga lace, ndi cocinjiriza cakonzeka.
6. Pa zipata za mitsinje patseguka, ndi cinyumba casungunuka.
7. Catsimikizika, abvulidwa, atengedwa, adzakazi ace alira ngati mau a nkhunda, nadziguguda pacifuwa pao.
8. Koma Nineve wakhala ciyambire cace ngati thamanda lamadzi; koma athawa. Imani, Imani! ati, koma palibe woceuka.