2. Yaphera nyama yace, nisanganiza vinyo wace,Nilongosolanso pa gome lace.
3. Yatuma anamwali ace, iitanaPa misanje ya m'mudzi.
4. Wacibwana yense apambukire kuno;Iti kwa yense wosowa nzeru,
5. Tiyeni, idyani cakudya canga;Nimumwe vinyo wanga ndamsanganiza.
6. Lekani, acibwana inu, nimukhale ndi moyo;Nimuyende m'njira ya nzeru.
7. Woweruza munthu wonyoza adzicititsa yekha manyazi;Yemwe adzudzula wocimwa angodetsa mbiri yace yace.
8. Usadzudzule wonyoza kuti angakude;Dzudzula wanzeru adzakukonda.
9. Ukacenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yace;Ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira,
10. Ciyambi ca nzeru ndico kuopa Yehova;Kudziwa Woyerayo ndiko luntha;