8. Mau a kazitape akunga zakudya zolongosoka,Zotsikira m'kati mwa mimba.
9. Wogwira nchito mwaulesiNdiye mbale wace wa wosakaza.
10. Dzina la Yehova ndilo linga lolimba;Wolungama athamangiramo napulumuka.
11. Cuma ca wolemera ndico mudzi wace wolimba;Alingalira kuti ndico khoma lalitari.
12. Mtima wa munthu unyada asanaonongeke;Koma cifatso citsogolera ulemu.
13. Wobwezera mau asanamvetse apusa,Nadzicititsa manyazi.
14. Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala;Koma ndani angatukule mtima wosweka?
15. Mtima wa wozindikira umaphunzira;Khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.
16. Mtulo wa munthu umtsegulira njira,Numfikitsa pamaso pa akuru.
17. Woyamba kudzinenera ayang'anika wolungama;Koma mnzace afika namuululitsa zace zonse.
18. Ula uletsa makangano,Nulekanitsa amphamvu.
19. Kupembedza mbale utamcimwira nkobvuta,Kulanda mudzi wolimba nkosabvuta;Makangano akunga mipiringidzo ya linga.
20. Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m'kamwa mwace;Iye nadzakhuta phindu la milomo yace.