1. Wopanduka afunafuna niro cace,Nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.
2. Wopusa sakondwera ndi kuzindikira;Koma kungobvumbulutsa za m'mtima mwace.
3. Pakudza wamphulupulu padzanso kunyoza;Manyazi natsagana ndi citonzo.
4. Mau a m'kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya;Kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.
5. Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankhu sikuli kwabwino,Ngakhale kucitira cetera wolungama.
6. Milomo ya wopusa ifikitsa makangano;Ndipo m'kamwa mwace muputa kukwapulidwa.
7. M'kamwa mwa wopusa mumuononga,Milomo yace ikhala msampha wa moyo wace.
8. Mau a kazitape akunga zakudya zolongosoka,Zotsikira m'kati mwa mimba.
9. Wogwira nchito mwaulesiNdiye mbale wace wa wosakaza.
10. Dzina la Yehova ndilo linga lolimba;Wolungama athamangiramo napulumuka.