1. Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo;Koma mau owawitsa aputa msunamo.
2. Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa;Koma m'kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru.
3. Maso a Yehova ali ponseponse,Nayang'anira oipa ndi abwino.
4. Kuciza lilime ndiko mtengo wa moyo;Koma likakhota liswa moyo.
5. Citsiru cipeputsa mwambo wa atate wace;Koma wosamalira cidzudzulo amacenjera.
6. M'nyumba ya wolungama muli katundu wambiri;Koma m'phindu la woipa muli bvuto,
7. Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru,Koma mtima wa opusa suli wolungama.
8. Nsembe ya oipa inyansa Yehova;Koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.
9. Njira ya oipa inyansa Yehova;Koma akonda wolondola cilungamo.
10. Wosiya njira adzalangidwa mowawa;Wakuda cidzudzulo adzafa.
11. Kumanda ndi kucionongeko kuli pamaso pa Yehova;Koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?
12. Wonyoza sakonda kudzudzulidwa,Samapita kwa anzeru.
13. Mtima wokondwa usekeretsa nkhope;Koma moyo umasweka ndi zowawa za m'mtima.
14. Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa;Koma m'kamwa mwa opusa mudya utsiru.
15. Masiku onse a wosauka ali oipa;Koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.