11. Cuma colandiridwa mokangaza cidzacepa;Koma wokundika ndi dzanja adzaona zocuruka.
12. Ciyembekezo cozengereza cidwalitsa mtima;Koma pakufika cifuniroco ndico mtengo wa moyo.
13. Wonyoza mau adziononga yekha;Koma woopa malangizo adzalandira mphotho.
14. Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo,Apatutsa ku misampha ya imfa.
15. Nzeru yabwino ipatsa cisomo;Koma njira ya aciwembu iri makolokoto.
16. Yense wocenjera amacita mwanzeru:Koma wopusa aonetsa utsiru.
17. Mthenga wolakwa umagwa m'zoipa;Koma mtumiki wokhulupirika alamitsa.