1. Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate;Koma wonyoza samvera cidzudzulo.
2. Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwace;Koma moyo wa aciwembu udzadya ciwawa.
3. Wogwira pakamwa pace asunga moyo wace;Koma woyasamula milomo yace adzaonongeka.
4. Moyo wa wolesi ukhumba osalandira kanthu;Koma moyo wa akhama udzalemera.
5. Wolungama ada mau onama;Koma woipa anyansa, nadzicititsa manyazi,
6. Cilungamo cicinjiriza woongoka m'njira;Koma udio ugwetsa wocimwa.
7. Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu;Alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi cuma cambiri.