17. Wacifundo acitira moyo wace zokoma;Koma wankhanza abvuta nyama yace.
18. Woipa alandira malipiro onyenga;Koma wofesa cilungamo aonadi mphotho,
19. Wolimbikira cilungamo alandira moyo;Koma wolondola zoipa adzipha yekha,
20. Okhota mtima anyansa Yehova;Koma angwiro m'njira zao amsekeretsa.
21. Zoonadi, wocimwa sadzapulumuka cilango;Koma mbeu ya olungama idzalanditsidwa.
22. Monga cipini cagolidi m'mphuno ya nkhumba,Momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.
23. Cifuniro ca olungama cifikitsa zabwino zokha;Koma ciyembekezo ca oipa mkwiyo.
24. Alipo wogawira, nangolemerabe;Aliponso womana comwe ayenera kupatsa nangosauka.
25. Mtima wa mataya udzalemera;Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.
26. Womana tirigu anthu amtemberera;Koma madalitso adzakhala pamtu pa wogulitsa.