16. Pakuti mapazi ao athamangira zoipa,Afulumira kukhetsa mwazi.
17. Pakuti kuchera msampha pamaso pa mbalame ndi cabe;
18. Ndipo awa abisalira mwazi wao wao, alalira miyoyo yao yao.
19. Mayendedwe a yense wopindula cuma monyenga ngotere;Cilanda moyo wa eni ace,
20. Nzeru ipfuula panja;Imveketsa mau ace pabwalo;
21. Iitana posonkhana anthu polowera pacipata;M'mudzi inena mau ace;
22. Kodi mudzakonda zacibwana kufikira liti, acibwana inu?Onyoza ndi kukonda kunyoza,Opusa ndi kuda nzeru?