Adzanyambita pfumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera poturuka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa cifukwa ca iwe.