Cifukwa cace atero Yehova, Taonani, ndilingirira coipa pa banja ili, cimene simudzacotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; Pakuti nyengo iyi ndi yoipa.