8. Koma udzapenya ndi maso ako,Nudzaona kubwezera cilango oipa.
9. Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo pangaUdaika Wam'mwambamwamba cokhalamo cako;
10. Palibe coipa cidzakugwera,Ndipo colanga sicidzayandikiza hema wako.
11. Pakuti adzalamulira angelo ace za iwe,Akusunge m'njira zako zonse.
12. Adzakunyamula pa manja ao,Ungagunde phazi lako pamwala.
13. Udzaponda mkango ndi mphiri;Udzapondereza msona wa mkango ndi cinjoka:
14. Popeza andikondadi ndidzampulumutsa;Ndidzamkweza m'mwamba, papeza adziwa dzina langa.
15. Adzandipfuulira Ine ndipo ndidzamyankha;Kunsautso ndidzakhala naye pamodzi;Ndidzamlanditsa, ndi kumcitira ulemu.
16. Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri,Ndi kumuonetsera cipulumutso canga,