1. Iye amene akhala pansi m'ngaka yace ya Wam'mwambamwambaAdzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
2. Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa;Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira,
3. Pakuti adzakuonjola ku msampha wa msodzi,Ku mliri wosakaza.
4. Adzakufungatira ndi nthenga zace,Ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ace;Coonadi cace ndico cikopa cocinjiriza.
5. Sudzaopa coopsa ca usiku, Kapena mubvi wopita usana;
6. Kapena mliri woyenda mumdima,Kapena cionongeko cakuthera usana.
7. Pambali pako padzagwa cikwi,Ndi zikwi khumi pa dzanja lamanja lako;Sicidzakuyandikiza iwe.
8. Koma udzapenya ndi maso ako,Nudzaona kubwezera cilango oipa.
9. Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo pangaUdaika Wam'mwambamwamba cokhalamo cako;