1. Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamoM'mibadwo mibadwo.
2. Asanabadwe mapiri,Kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu,Inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha,Inu ndinu Mulungu.
3. Mubweza munthu akhale pfumbi;Nimuti, Bwererani inu, ana a anthu.
4. Pakuti pamaso panu zaka zikwiZikhala ngati dzulo, litapita,Ndi monga ulonda wa usiku.
5. Muwatenga ngati ndi madzi akulu, akhala ngati tulo;Mamawa akhala ngati msipu waphuka.
6. Mamawa uphuka bwino;Madzulo ausenga, nuuma.