3. Pakuti mzimu wanga wadzala nao mabvuto,Ndi moyo wanga wayandikira kumanda.
4. Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje;Ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu:
5. Wotayika pakati pa akufa,Ngati ophedwa akugona m'manda,Amene simuwakumbukilanso;Ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.
6. Munandiika kunsi kwa dzenje,Kuti mdima, kozama.
7. Mkwiyo wanu utsamira pa ine,Ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.