7. Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyesa Mulungu mphamvu yace;Amene anatama kucuruka kwa cuma cace,Nadzilimbitsa m'kuipsa kwace.
8. Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi waazitona m'nyumba ya Mulungu:Ndikhulupirira cifundo ca Mulungu ku nthawi za nthawi.
9. Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munacicita ici:Ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ici ncokoma, pamaso pa okondedwa anu,