2. Awamba ndi omveka omwe,Acuma ndi aumphawi omwe.
3. Pakamwa panga padzanena zanzeru;Ndipo cilingiriro ca mtima wanga cidzakhala ca cidziwitso.
4. Ndidzachera khutu kufanizo:Ndidzafotokozera cophiphiritsa canga poyimbira.
5. Ndidzaoperanji masiku oipa,Pondizinga amphulupulu onditsata kucidendene?
6. Iwo akutama kulemera kwao;Nadzitamandira pa kucuruka kwa cuma cao;
7. Kuombola mbale sangadzamuombole,Kapena kumperekera dipo kwa Mulungu:
8. (Popeza ciombolo ca moyo wao nca mtengo wace wapatali,Ndipo cilekeke nthawi zonse)
9. Kuti akhale ndi moyo osafa,Osaona cibvundi.