5. Mibvi yanu njakuthwa;Mitundu ya anthu igwa pansi pa Inu:Iwalasa mumtima adani a mfumu.
6. Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ukhala nthawi zonse zamkamuyaya:Ndodo yacifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.
7. Mukonda cilungamo, ndipo mudana naco coipa:Cifukwa cace Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inuNdi mafuta a cikondwerero kuposa anzanu.
8. Zobvala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasya;M'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njobvu mwatoruka zoyimba za zingwe zokukondweretsani.
9. Mwa omveka anu muli ana akazi amafumu:Ku dzanja lamanja lanu aima mkazi wa mfumu wobvala golidi wa ku Ofiri.
10. Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tachera khutu lako;Uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;
11. Potero mfumuyo adzakhumba kukoma kwako:Pakuti ndiye mbuye wako; ndipo iwe umgwadire iye.