11. Potero mfumuyo adzakhumba kukoma kwako:Pakuti ndiye mbuye wako; ndipo iwe umgwadire iye.
12. Ndipo mwana wamkazi wa Turo adzafika nayo mphatso;Acuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.
13. Mwana wamkazi wa mfumu ngwa ulemerero wonse m'kati mwa nyumba:Zobvala zace nza made agolidi.
14. Adzamtsogolera kwa mfumu wabvala zamawanga-mawanga:Anamwali anzace omtsata adzafika nao kwa inu.
15. Adzawatsogolera ndi cimwemwe ndi kusekerera:Adzalowa m'nyumba ya mfumu.
16. M'malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako,Udzawaika akhale mafumu m'dziko lonse lapansi.
17. Ndidzawakumbutsa dzina lanu m'mibadwo mibadwo:Cifukwa cace mitundu ya anthu idzayamika Inu ku nthawi za nthawi.