1. Mtima wanga usefukira naco cinthu cokoma:Ndinena zopeka ine za mfumu:Lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.
2. Inu ndinu wokongola ndithu kuposa ana a anthu;Anakutsanulirani cisomo pa milomo yanu:Cifukwa cace Mulungu anakudalitsani kosatha.
3. Dzimangireni lupanga lanu m'cuuno mwanu, wamphamvu inu,Ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu.
4. Ndipo pindulani, m'ukulu wanu yendani,Kaamba ka coonadi ndi cifatso ndi cilungamo:Ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.
5. Mibvi yanu njakuthwa;Mitundu ya anthu igwa pansi pa Inu:Iwalasa mumtima adani a mfumu.
6. Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ukhala nthawi zonse zamkamuyaya:Ndodo yacifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.