Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazicita nzambiri,Ndipo zolingirira zanu za pa ife;Palibe wina wozifotokozera Inu;Ndikazisimba ndi kuzichula, Zindicurukira kuziwerenga.