1. Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu:Ndipo musandilange moopsa m'mtima mwanu.
2. Pakuti mibvi yanu yandilowa,Ndi dzanja lanu landigwera.
3. Mumnofu mwanga mulibe camoyo cifukwa ca ukali wanu;Ndipo m'mafupa anga simuzizira, cifukwa ca colakwa canga.
4. Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga:Ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.
5. Mabala anga anunkha, adaola, Cifukwa ca kupusa kwanga.
6. Ndapindika, ndawerama kwakukuru;Ndimayenda woliralira tsiku lonse.
7. Pakuti m'cuuno mwanga mutentha kwambiri;Palibe pamoyo m'mnofu mwanga,
8. Ndafoka ine, ndipo ndacinjizidwa:Ndabangula cifukwa ca kumyuka mtima wanga.