4. Cifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine;Uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.
5. Ndinabvomera coipa canga kwa Inu;Ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa.Ndinati, Ndidzaululira Yehova macimo anga;Ndipo munakhululukira coipa ca kulakwa kwanga.
6. Cifukwa cace oyera mtima onse apemphere kwa Inu,Pa nthawi ya kupeza Inu:Indetu pakusefuka madzi akuruSadzamfikira iye.
7. Inu ndinu mobisalira mwanga; M'nsautso mudzandisunga;Mudzandizinga ndi Nyimbo za cipulumutso.
8. Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo;Ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
9. Musakhale monga kavalo, kapena ngati buru, wopanda nzeru:Zomangira zao ndizo cam'kamwa ndi capamutu zakuwakokera,Pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.
10. Zisoni zambiri zigwera woipa:Koma cifundo cidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.
11. Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima;Ndipo pfuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.