1. Wodala munthuyo wokhululukidwa chimo lace;Wokwiriridwa coipa cace.
2. Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zace;Ndimo mumzimu mwace mulibe cinyengo.
3. Pamene ndinakhala cete mafupa anga anakalambaNdi kubuula kwanga tsiku lonse.
4. Cifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine;Uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.