5. Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza;Inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebano.
6. Aitumphitsa monga mwana wa ng'ombe;Lebano ndi Sirio monga msona wa njati.
7. Liu la Yehova ligawa malawi a moto.
8. Liu la Yehova ligwedeza cipululu;Yehova agwedeza cipululu ca Kadese.
9. Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi,Ndipo lipulula nkhalango:Ndipo m'Kacisi mwace zonse ziri m'mwemo zimati, Ulemerero:
10. Yehova anakhala pa Cigumula:Inde Yehova akhala mfumu ku nthawi yomka muyaya.
11. Yehova adzapatsa anthu ace mphamvu:Yehova adzadalitsa anthu ace ndi mtendere.