7. Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi cikopa canga;Mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza:Cifukwa cace mtima wanga ukondwera kwakukuru;Ndipo ndidzamyamika nayo Nyimbo yanga.
8. Yehova ndiye mphamvu yao,Inde mphamvu ya cipulumutso ca wodzozedwa wace.
9. Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa colandira canu:Muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.