Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga;Ndipo ndidzapereka m'cihema mwace nsembe za kupfuula mokondwera;Ndidzayimba, inde, ndidzayimbira Yehova zomlemekeza.