3. Tidule zomangira zao,Titaye nsinga zao.
4. Wokhala m'mwambayo adzaseka;Ambuye adzawanyoza.
5. Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wace,Nadzawaopsa m'ukali wace:
6. Koma Ine ndadzoza mfumu yangaPa Ziyoni, phiri langa loyera.
7. Ndidzauza za citsimikizo:Yehova ananena ndiIne, Iwe ndiwe Mwana wanga;Ine lero ndakubala.
8. Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale colowa cako,Ndi malekezero a dziko lapansi akhale ako ako.