9. Kundilanditsa kwa oipa amene andipasula,Adani a pa moyo wanga amene andizinga.
10. Mafuta ao awatsekereza;M'kamwa mwao alankhula modzikuza.
11. Tsopano anatizinga m'mayendedwe athu:Apenyetsetsa m'maso kuti atigwetse pansi.
12. Afanana ndi mkango wofuna kumwetula,Ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo.
13. Ukani Yehova,Mumtsekereze, mumgwetse:Landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;
14. Kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova,Kwa anthu a dziko lapansi pano amene colowa cao ciri m'moyo uno,Ndipo mimba yao muidzaza ndi cuma canu cobisika:Akhuta mtima ndi ana,Nasiyira ana amakanda zocuruka zao.
15. Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'cilungamo:Ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.