4. Penyani ku dzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa;Pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.
5. Ndinapfuulira kwa inu, Yehova;Ndina, Inu ndinu pothawirapo panga,Gawo langa m'dziko la amoyo.
6. Tamverani kupfuula kwanga; papeza ndisauka kwambiri;Ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andilaka.
7. Turutsani moyo wanga m'ndende, kuti ndiyamike dzina lanu;Olungama adzandizinga;Pakuti mudzandicitira zokoma.