21. Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova?Ndipo kodi sindimva nao cisoni iwo akuukira Inu?
22. Ndidana nao ndi udani weni weni:Ndiwayesa adani.
23. Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga;Mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.
24. Ndipo mupenye ngati ndiri nao mayendedwe oipa,Nimunditsogolere pa njira yosatha.