1. Yehova, kumbukilani Davide Kuzunzika kwace konse;
2. Kuti analumbira Yehova,Nawindira Wamphamvuyo wa Yakobo, ndi kuti,
3. Ngati ndidzalowa pakhomo pa nyumba yanga,Ngati ndidzakwera pa kama logonapo;
4. Ngati ndidzalola maso anga agone,Kapena zikope zanga ziodzere;