1. Wodala yense wakuopa Yehova, Wakuyenda m'njira zace.
2. Pakuti udzadya za nchito ya manja ako;Wodala iwe, ndipo kudzakukomera.
3. Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako;Ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.
4. Taonani, m'mwemo adzadalitsikaMunthu wakuopa Yehova.
5. Yehova adzakudalitsa ali m'ZiyoniNdipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.
6. Inde, udzaona zidzukulu zako.Mtendere ukhale ndi Israyeli.
Werengani mutu wathunthu Masalmo 128