19. Nditsegulireni zipata za cilungamo;Ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova.
20. Cipata ca Yehova ndi ici;Olungama adzalowamo.
21. Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha,Ndipo munakhala cipulumutso canga,
22. Mwala umene omangawo anaukanaWakhala mutu wa pangondya.
23. Ici cidzera kwa Yehova;Ncodabwiza ici pamaso pathu.
24. Tsiku ili ndilo adaliika Yehova;Tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.
25. Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano;Tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.
26. Wodala wakudzayo m'dzina la Yehova;Takudalitsani kocokera m'nyumba ya Yehova.
27. Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira;Mangani nsembe ndi zingwe, ku nyanga za guwa la nsembe.
28. Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;Ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani.
29. Yamikani Yehova, pakuti Iye ndiye wabwino,Pakuti cifundo cace ncosatha.