9. Ana ace akhale amasiye, Ndi mkazi wace wamasiye.
10. Ana ace akhale amcirakuyenda ndi opemphapempha;Afunefune zosowa zao kucokera m'mabwinja mwao.
11. Wokongoletsa agwire zonse ali nazo;Ndi alendo alande za nchito yace.
12. Pasakhale munthu wakumdtira cifundo;Kapena kucitira cokoma ana ace amasiye.
13. Zidzukulu zace zidulidwe;Dzina lao lifafanizidwe mu mbadwo ukudza.
14. Mphulupulu za makolo ace zikumbukike ndi Yehova;Ndi cimo la mai wace lisafafanizidwe.
15. Zikhale pamaso pa Yehova cikhalire,Kuti adule cikumbukilo cao kucicotsera ku dziko lapansi.