22. Pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi,Ndi mtima wanga walaswa m'kati mwanga.
23. Ndamuka ngati mthunzi womka m'taliNdiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.
24. Mabondo anga agwedezeka cifukwa ca kusala;Ndi mnofu wanga waonda posowa mafuta.
25. Ndiwakhaliranso cotonza;Pakundiona apukusa mutu.
26. Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga:Ndipulumutseni monga mwa cifundo canu;
27. Kuti adziwe kuti ici ndi dzanja lanu;Kuti Inu Yehova munacicita.
28. Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu;Pakuuka iwowa adzacita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera.
29. Otsutsana nane abvale manyazi,Nadzikute naco cisokonezo cao ngati ndi copfunda.
30. Ndidzayamika Yehova kwakukuru pakamwa panga;Ndi pakati pa anthu aunyinji ndidzamlemekeza.
31. Popeza adzaima pa dzanja lamanja la waumphawiKumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wace.