1. Mulungu wa cilemekezo canga, musakhale cete;
2. Pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa cinyengo pananditsegukira;Anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza.
3. Ndipo anandizinga ndi mau a udani,Nalimbana nane kopanda cifukwa.
4. M'malo mwa cikondi canga andibwezera udani;Koma ine, kupemphera ndiko.
5. Ndipo anandisenza coipa m'malo mwa cokoma,Ndi udani m'malo mwa cikondi canga.
6. Muike munthu woipa akhale mkuru wace;Ndi mdani aime pa dzanja lamanja lace.
7. Ponenedwa mlandu wace aturuke wotsutsika;Ndi pemphero lace likhale ngati kucimwa.
8. Masiku ace akhale owerengeka;Wina alandire udindo wace.
9. Ana ace akhale amasiye, Ndi mkazi wace wamasiye.
10. Ana ace akhale amcirakuyenda ndi opemphapempha;Afunefune zosowa zao kucokera m'mabwinja mwao.
11. Wokongoletsa agwire zonse ali nazo;Ndi alendo alande za nchito yace.
12. Pasakhale munthu wakumdtira cifundo;Kapena kucitira cokoma ana ace amasiye.
13. Zidzukulu zace zidulidwe;Dzina lao lifafanizidwe mu mbadwo ukudza.
14. Mphulupulu za makolo ace zikumbukike ndi Yehova;Ndi cimo la mai wace lisafafanizidwe.