17. Ndipo anabwera nayo nsembe yaufa, natengako wodzala dzanja, nautentha pa guwa la nsembe, angakhale adatentha nsembe yopsereza ya m'mawa.
18. Anaphanso ng'ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozungulira, ndi mafuta a ng'ombe;
19. ndi a nkhosa, ndi mcira wamafuta, ndi cophimba matumbo, ndi imso, ndi cokuta ca mphafa;
20. ndipo anaika mafuta pa ngangazo, natentha mafutawo pa guwa la nsembe.
21. Ndipo Aroni anaweyula ngangazo ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; monga iye anauza Mose.