Pamenepo Mose anazicotsa ku manja ao, nazitentha pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza; ndizo nsembe zodzaza manja zocita pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.